Stay updated with our latest news, announcements, and events
We are not politically affliated
November 16, 2025
Akuluakulu a bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition HRDC, atsutsa mphekesera zoti bungweli limagwira ntchito ndi chipani cha Malawi Congress MCP.
Poyankhula pa mkumano wa olemba nkhani ku Lilogwe, wapampando wa bungweli Michael Kaiyatsa, wati iwo amagwira ntchito yomenyera ufulu wa anthu posatengera boma lomwe likulamula.
Kaiyatsa watsutsanso mphekesera zoti iwo akufuna kupanga ziwonetsero zosenyeza kusakondwa ndi boma latsopano lotsogozedwa ndi chipani cha Democratic Progress DPP, ponena kuti iwo sapanga ziwonetsero mwachisawawa komanso popanda chifukwa chenicheni.
Iye wati nkhani zambiri za bodza zomwe zikukambidwa m'masamba amchezo ndizongofuna kuipitsa mbiri ya bwino ya bungweli zomwenso zikupangitsa kuti ambiri mwa ma membela awo adzikhala mwa mantha.
Pakadalipano, Kaiyatsa walengeza kukhazikitsidwa kwa ntchito yatsopano pansi pa bungweli yomwe cholinga chake ndi kuteteza omenyera ufulu wa anthu omwe akukumana ndi zovuta monga chitetezo komanso thandizo ku mabwalo a milandu mwazina.
Comments (0)
No comments yet. Be the first to comment!